SO FAR UTM HAS HOSTED MORE THAN 20 RALLIES AFTER CONSTITUTIONAL COURT RULING
By Chikumbutso Willard
Pamene dziko lino likuyembekezera kuponyatso voti ya mpando wa pulezidenti mu miyezi isanu ikubwerayi, zikuwonesa kuti chipani cha UTM ndichokhacho chatanganidwa ndikuchititsa misonkhano yokopa anthu.
Bwalo la milandu litagamula kuti anthu azaponyeso voti pa mpando wa pulezidenti, Chipani cha UTM sichinadikire khelere losonyeza kuti ayambepo kupanga misonkhano yokopa anthu ayi, iyo yagundika kuchitisa misonkhano m’madera osiyanasiyana m’dziko muno.
Mosogozedwa ndi wachiwiri kwa pulezidenti wa chipanichi Dr Michael Usi komanso Mlembi wankulu wa UTM mayi Patricia Kaliati, UTM yadya matako agalu ikukanika kukhala pansi mmalo mwake akuchitsa misonkhano mdziko muno.
Dzulo pa 16 February 2020,UTM inali ndi mitsokhano iwiri yomwe kunali chinatindi chawanthu.
A Dr Michael Usi ndi ena akulu akulu achipani anali ku Mwanza komwe anapangitsa msonkhano.


A Usi anathokoza anthu onse pazomwe anachita povotela chipani cha UTM komaso anawalimbikitsa anthuwo powawunikila zolinga za chipani chawocho.

Nawo Mayi Kaliati sanaonetse kutopa koma kukachitisa msonkhano pa bwalo la Chibambo ku Mzuzu.Iwo anali ndi akuluakulu achipani monga Mr C.Malunga,RG Njikho,Mai Bridget Nkhoma,Makwenda Chunga,Mai Loveness Gondwe ndi ena ambili.
Komaso a Rev aku Livingstonia synod and mafumu ochulukaso.
Mai Kaliati anawapepesa anthu omwe anasokhanawo kamba kokuti boma lalephela kuwapatsa zofunikila monga Jenda/jagwa mseu,milatho ya salima/nkhotakota,engweni,chakazi ndi masukulu ambili akanika kumanga monga Mombera ndi Mzuzu university,masitiyediyamu monga mzimba,mzuzu komaso ma office abwana kubwa ku mzimba.
Komaso anawathokoza anthu onse chifukwa cha support yawo povotela utm padzitsakho zapitazi.
Ayi,ndithu a utm akuyesesa kufikila Amalawi ponse ponse,konse komwe ali.
DPP komanso MCP iwo sanayambe kuchitisa misonkhano,khoti chipelekereni chigamulo pa 3 February chaka chino. MCP yokha ndiyomwe inapangitsa msonkhano wothokoza anthu kwa Msundwe ku Lilongwe tsabata latha koma ku DPP kuli ziii.

Way cool! Some extremely valid points! I appreciate you writing this write-up and
also the rest of the site is extremely good.