“PALIBE ANGATI INE NDINAWINA UPULEZIDENTI PAZITSAKHO ZA 2019,MUKAMUVA ZIWANI NDIWABOZA” BAMBO CHILIMA ATERO
Pulezidenti wachipani cha UTM ameneso ali tsogoleri wachiwiri mudziko lino Bambo Saulos Klaus Chilima anayakhula mosapsyatila mau.Iwo amapangitsa tsokhano ku bwalo lamasitha ku Lilongwe,muchigawo chapakati.
Achilima ananenetsa kuti “Amalawi musanamizidwe,palibe yemwe angayime pachulu ndikutha mau kuti iye ndiye anawina zitsakho za 2019 ngati pulezidenti,limenelo ndi bodza la mtu wagalu.Anthu odziwa malamulo omwe anapeleka chigamulo,anati zonse zakale zafwafwanizidwa;!apapa palibe amene ali mavoti ochuluka kuposa wina,tonse tili ku zero basi.”
Iwo anawonjezera mau ” amalawi dekhani,nkhani ya gwirizano tikuyitsatila bwino lomwe ndipo musakhale pachangu;kodi gwirizano ukuyenela kukhala okomela amalawi osati zipani,komaso mugwirizanomo mukuyenela kukhala kugwirizana”
Achilima akuyembekezela kupanganso mitsokhano madela ena akuvuma ndi kumpoto.
