NKHANI ZA TSABATA LAPITALI MWACHINDUNJI.

WhatsApp Video 2020-08-10 at 09.37.15

NKHANI

Gulu lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition HRDC lalemba chikalata chopita kwa mkulu wa Malawi Broadcasting Corporation ( MBC) kupempha MBC kuti iwapepese chifukwa chowatchula kuti HRDC ndi gulu la zifwamba komanso HRDC ikufuna MBC iwapatse Mk 200 miliyoni ngati chipepeso powanyoza komanso powayipitsira mbiri, HRDC yawopseza kuti itengera MBC Ku khothi pakadutsa masiku 7 ngati MBC inyozere zomwe HRDC ikufuna.


-Mtsogoleri wa dziko lino Prof Peter Mutharika anena kuti ali okonzeka kukomana ndi atsogoleri a zipani zosusa boma kuti athe kukambilana zozetsa mtendere kuti mpungwepungwe omwe ukuchitika mdziko la Malawi uthe iwo apempha amalawi kuti asiye kupanga ziwonetsero. Iwo ayakhula izi dzulo pomwe amanyamuka kupita Ku London Ku United Kingdom Ku msonkhano waza malamulo wa pakati pa dziko la United Kingdom ndi azitsogoleri amu Africa.

-Apolisi ku Nkhotakota amanga group village headman Chioza chifukwa chogwililila msungwana wa zaka zakubadwa 11.

-Kampani ya central poultry limited Ku Mpingu yati nkhuku zokwana 14,448 zabedwa ku mpingu breeder farm ku Lilongwe dzana pamene anthu amapanga ziwonetsero za HRDC anapita Ku kampaniyo ndikunyamula nkhuku pamodzi ndi mazila kuphatikizaponso katundu wina

-Apolisi ku Dedza amanga mneneri wachikazi kapena kuti prophetess yemwe amanena kuti waukisa munthu wakufa. Iye anati mnyamata wa zaka zakubadwa 14 yemwe anafa pa ngozi yapansewu mchaka cha 2016 waukisidwa ndi iyeyo.

-Bungwe la Malawi Electoral Commission MEC lalengeza kuti Zisankho za padera/ by-election zosankha phungu wa nyumba ya malamulo ku dera la kum’mwera mu mzinda wa Lilongwe zichitika pa 30 January 2020. Chipani cha UTM chanena kuti sichitenga nawo gawo pa zisankhozo ponena kuti adataya chikhulupiliro mwa bungwe la MEC.

-Mamuna wa zaka zakubadwa 35 ku Ntchisi wazipha pozimangilila lachiwiri lapitali atazindikila zoti mkazi wake amamudabula kapena kuti amachita zibwenzi ndi amuna ena

-Nduna yowona za ulimi a Kondwani Namkumwa ali Ku Berlin m’dziko la German Ku msonkhano wokhuza za ulimi ndi Chakudya ( 2020 Global Forum On food and Agriculture) womwe unayamba dzana pa 16 ndipo utha lero pa 18 January 2020.

-Asilikali ankhondo a MDF mothanizana ndi apolisi la chinayi analanda ma lorry okwana 14 omwe amanyamula anthu kupita ku malo komwe kumachitikila zioneselo ponena kuti sanali oyenela kuyenda pa msewu komanso amanyamula anthu popanda chilolezo cha ku police, Anthuwo amachokera kwa Msundwe.

-Mabanja 3,954 m’boma la Phalombe akusowa pokhala chifukwa choti nyumba zawo zidagwa kamba ka madzi osefukira zomwe zadza chifukwa cha mvula yamphamvu yomwe yakhala ikugwa m’bomalo.

-Apolisi ku chitipa lachitatu amanga anthu 18 omwe anathyola ma shop ndikuba katundu osiyanasiyana pa zioneselo zomwe zinachitika sabata yatha ku delalo.

-Apolisi ku Phalombe amanga anthu 9 chifukwa chokumba msewu wa tala omwe wangomangidwa kumene wa Zomba – Jali – Phalombe popanga njira ya madzi osefukira popita tsidya lina la msewu.

-Matope omwe anaza chifukwa cha kusefukila kwa madzi mdziko la Pakistan akwilila nyumba zambiri za anthu ku Himalayan region ku Neelam valley komwe anthu 77 aphedwa.

-Dziko la USA lati asilikali ankhondo a dziko la USA okwana 11 ndi omwe anavulala pa mabomba omwe dziko la Iran linaponya ku Iraq pa 8 January 2020. Poyamba dziko la USA linakana zoti palibe yemwe wavulala pa chiwembucho.

-Anthu oposa 100 aphedwa mdziko pa Pakistan pamene mafunde a snow anapangisa kuyenda kwa nthaka ndipo anaononga midzi ingapo.

-Nyumba ya malamulo mdziko la USA yatsegula mulandu wa President wa dzikolo a Donald Trump. Mkulu wa malamulo a John Roberts analumbila kuti atsogolere ntchito yoweruza mulandu pa milandu yofuna kuchotsa pampando President wa dziko la USA a Donald Trump.

Yamikani Kachingwe

Yamikani Nicholas Kachingwe is a Malawian with great interest in current affairs, news and storytelling. Over the years, he has established himself as a a great source of news, a private investigator of issues and whistle blower using various social media platforms.

18 thoughts on “NKHANI ZA TSABATA LAPITALI MWACHINDUNJI.

Comments are closed.